Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine-logo

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine

Religion & Spirituality Podcas

Sermons and teaching in Chichewa and English

Location:

United States

Description:

Sermons and teaching in Chichewa and English

Language:

English


Episodes
Ask host to enable sharing for playback control

John 6:60-71| Are you a true disciple of Jesus Christ? by Pastor M. Kuthyola

5/22/2024
Pastor Kuthyola has been pastoring Unity Bible Church which meet at T&D near Chanco University in Zomba. on this sermon he laboured to exposit the text in providing the marks of a true disciple. As a true disciple

Duration:00:48:45

Ask host to enable sharing for playback control

Roman 12:14-21| How to Biblically respond to hurt? by Pastor P. Chibwana.

5/21/2024
Pastor Chibwana has been pastoring Mulunguzi Community Church at Matawale in Zomba for many years. He has been preaching expository sermons from the book of Romans. In this sermon, he labours to explain how believers are to respond when hurting by offering four ways to the body of Christ namely: Please listen, and if you have any questions you may ask through our podcast and we should be able to address those questions.

Duration:01:05:57

Ask host to enable sharing for playback control

Cholinga cha lamuloli ndi chikondi/The aim of the charge is love

4/9/2024
1 Timoteyo 1:5-7 m’mavesi amenewa, Paulo mtumwi akuonetsera kufunika kolalikira mawu a mulungu kwa anthu. Iye akunena kuti ndi lamulo lochokera kwa olamulira wamkulu limene limaperekedwa kwa abusa onse omwe ali mchoonadi. Yesu monga iye mwini ulamuliro, akulamulira abusa onse kuti alalikire mawu a mulungu mpaka kumalekezero adziko lapansi kenako mathero azafika. M’busa kuti alalikire, akuyenera kukhala ndi chikondi pa anthu omwe akuwalalikira komanso amve kusoweka komwe anthu alinako kofunikira chipulumutso. Nchifukwa chake tinganene kuti cholinga cha lamuloli ndi chikondi monga momwe Paulo mtumwi akuyankhulira. 1 Timothy 1:5-7 in these verses, the apostle Paul puts emphasis on the need to preach the word of God to people. He says that it is a charge that all true pastors receive from higher authority. Jesus as the one with authority, he charges all pastors to preach the word of God to the ends of the earth and then the end will come. But for a true pastor to preach, he must have deep love for God’s people and feel the need to rescue them all through the preaching of the gospel. Therefore, we can conclude to say that the aim of the charge is love as the apostle Paul puts it.

Duration:00:30:56

Ask host to enable sharing for playback control

Kusiyana pakati pa mpingo wa chikhalidwe ndi mpingo wa akhristu/The differences between traditional churches and Christian churches

2/11/2024
Mateyu 5:38-42 ikutionetsera kusiyana kwa pakati pa maweruzidwe a dziko lapansi ndi a nkhristu yemwe walakwiridwa. Dziko limalimbikitsa kubwenzera pamene ena atilakwira ife. Mwachitsanzo, pamene wina amenya tsaya lako, nawenso umenye lake. Dziko limanena kuti mupatse anthu zomwe zikuwayenereza pomwe achita choyipa. Koma umu sim’mowe okhulupirira akuyenera kukhalamo. Timakhala munjira yosiyana ndi dziko lapansi. Yesu akutiuza kuti tipatse anthu zomwe sakuyenera panthawi yomwe atichitira zoyipa. Pamene wina sanachite bwino, m’malo momubwenzera, tiyenera kumukonda. Nchifukwa chiyani tiwakonde? Chifukwa talandira chinthu china chabwino. Talandira chifundo cha mulungu ndi chifukwa timaonetsera chifundo. Pamapeto pa zonse, mulungu ndi mwini kuweruza ndipo azaweruza. Tikungoyenera kumudalira. Mathew 5:34-42 is showing us the differences between the worldly ways of judging and the way a Christian reacts when mistreated. The world would tell you to fight back when someone has done something wrong to you. For example, slapping you on the chick, you also slap back. The world would tell you to give people what they deserve when in the wrong. But, that’s not how a true believer should live. We live in such a way that is different from this world. Jesus tells us to give people what they do not deserve when they are in the wrong. If someone has done you injustice, instead of revenging, he tells us to show them love. Why should we love them? because we have we received something better. We have received the mercy of God and that’s why we show mercy. At the end of the day, God is the judge of everything and surely, he will deliver justice and we just need to trust him.

Duration:00:38:15

Ask host to enable sharing for playback control

Zoyenera kudziwa potsuzula mkazi/what to know about divorcing your wife

1/29/2024
Mateyu 5:31, 32 ndizomvetsa chisoni kuona mawanja ambiri akutha chifukwa cha zifukwa zosaziwika bwino. Mabanja ambiri tsiku lalero akumangidwa pa madziko opanda pake. Nthawi zina, ena akumanga mabanja chifukwa mwina mtsikana wapatsidwa mimba, ena akuyamba banja chifukwa chofuna kukwanilitsa zakuthupi, akufuna kukwanilitsa zokhumba zogonana. Ngati zotsatira za izi, mabanja ambiri akutha. Mabanja ambiri akusuzurana. Mu ndime yamalemba iyi, tikuona chifukwa chomveka bwino chimene munthu ali ndikuthekera komutsuzula mkazi kapena m’bambo m’banja. Tikuuzidwa kuti ngati mkazi wagwidwa ndi chigololo akhoza kutsuzulidwa. Ngati izi zichitika mosemphana ndi lamuloli, mkaziyo amasandutzidwa pochitira chigololo. Ngakhale pali zina zovutitsitsa kwambiri m’banja monga ngati nkhondo m’banja, kunena kuti ngati chitsudzulo sichiperekedwa mwina moyo ukhoza kutayidwa pamenepo chitsudzulo chitha kuperekedwa. Mathew 5:31, 32 it is very sad to see many marriages falling apart because of selfish reasons. Many marriages today are based on foolish foundations. Sometimes, others are starting a marriage because the girl is pregnant, others are starting a marriage on the basis of pleasures, they want to satisfy their sexual desires in marriage. Due to these foolish reasons, many marriages are falling apart. Many are divorcing today. But, in this passage we see the only reason a man or woman is legible enough to divorce his wife or her husband. The passage tells us that the only grounds for divorce in marriage is sexual immorality. Jesus says that “whoever divorces his wife except on the grounds of sexual immorality, commits adultery. And whoever marries a divorced wife commits adultery.” This is the only reason that is given on the grounds for divorce. But there are other reasons for divorcing, and are legal. For example, on circumstances of physical assault in a marriage, that if divorce is not given then a life may be lost, then divorce may be permissible.

Duration:00:37:45

Ask host to enable sharing for playback control

Pewani kusilira/Abstain from Lusting

1/22/2024
Mateyu 5:27-30 kuzitukumula, ulesi, kukonda ndalama ndi mayesero opezeka paliponse pakati abusa omwe akusamalira nkhosa za mulungu. Kusilira ndi yesero lomwe ndi loopsa pa onse. Chifukwa chiyani zili choncho? Ndikovuta kubwerera kuvutoli ndi kukhalabe m’busa oyang’anira nkhosa za mulungu. M’busa akalephera mbali imeneyi amakhala osayenera kukhalanso m’busa wa nkhosa za mulungu kwa moyo wake wonse. Yesu ananena kuti, munamva kuti “usachite chigololo koma ndikuuza kuti yense amene ayang’ana mzimayi ndi kumusilira wachita naye kale chigololo.” Yesu akukhwimitsa malamulo a mulungu poyankhula zimenezi. Iye achita izi chifukwa amalabadira zomwe zili mumtima mwathu. Ngati uyang’ana mzimayi ndi kumusilira wachita naye kale chigololo. Yesu akufuna ife kuti timvetse bwino komwe kuli vuto, ndipo vuto ndi mtima wathu. Ntchito iliyonse imene imachitika imayamba ndi khumbo lochokera mumtima. Tiyenera kukhala atcheru ndi osamalisa ndi zokhumba za mtima wathu pamene tikuyang’anira nkhosa za mulungu. Mathew 5:27-30 Pride, laziness, love of money are common temptations that pastors who are shepherding God’s flock have. But lusting is the most dangerous temptation of them all. Why is that? It is almost impossible to recover from it and remain a pastor of God’s flock. You fail in this part of your life, you will be disqualified for the rest of your life from the ministry of pastoring God’s people. Jesus says, you heard it say “do not commit adultery, but I tell you that whoever looks at a woman so as to have sexual passion for her has already committed adultery with her in his heart.” Jesus raises the bar here. He does so because he cares about inward standards of our hearts. If you look at a woman lustfully you commit adultery with her. Jesus wants us to understand where the problem is and the problem is the desires of our hearts. Every action that is committed begins with the desire in the heart. So, it is important that we safe guard our hearts as we are looking after God’s people.

Duration:00:51:58

Ask host to enable sharing for playback control

Kodi mpingo wabwino ndi wotani? What is the best Church?

1/17/2024
Akolose 1:3-8 chaputa ichi chikuwonetsa makhalidwe asanu ndi chimodzi a mpingo wabwino. Choyamba ndi mbiri yabwino. Mutakhala kuti mwafunsidwa funso kuti mufotokoze mbiri ya mpingo wanu, inu munganene kuti chiyani? Kodi munganene kuti mulungu akugwira ntchito mu mpingo mwanu? Chinthu china ndi chidwi cha mpingo pa Yesu. Kodi mpingo wanu uli ndi chidwi chonse pa Yesu mu zonse? Ndipo chidwi chake ndi choposa? Nankha kodi mpingo wanu umakonda munjira yomwe ndi mulungu yekha angafotokoze? Makhalidwe anu kodi akuonetsa kuti muli okonzeka kukhala kumwamba? Kodi uthenga wabwino ukubereka zipatso mwa inu? Kodi mpingo ukutengera anthu kwa Yesu? Zinthu zonena zilipo zmbiri koma chinthu chofunika kumvetsa ndi chakuti mpingo si nyumba yokongolayo, kapena zovala zokongola zomwe akhristu amavalazo kapena chilichonse chokhuzana ndi dziko lapansi. Mpingo ndi zinthu za mulungu zomwe zakambidwa mwambamu, zimenezo ndi zomwe zimapanga mpingo weniweni. Colossians 1:3-8 this chapter displays six characters of a good church. The first is reputation. If you were to be asked about the reputation of your church, what would you say? Would you say that God is at work in the church? Another character is church focus on Jesus. Is your church fully engaged and focused on Jesus? Can we say it is Laser focused on Jesus alone? Does the church love in such a way that only God can explain it? And what about the life style, does it show that you live for heaven? Is the gospel bearing fruits in you? Is the church doing all it can to bring people to Jesus? The list goes on and on but what is important is that we understand that church is not about the nice building, nice clothes you wear when going to church or anything worldly but the things of God. And that makes a real church.

Duration:00:28:48

Ask host to enable sharing for playback control

Yesu Khristu mwini Chilamulo komanso mpulumutsi wa anthu onse/Jesus Christ the fulfilment of the law and savior of all people

1/2/2024
Luka 2:21-35 ndime ya malembayi ikukamba zinthu zingapo zomwe ndizofunika kuzikamba. Ndimeyi ikukamba zokhuza Yesu kukhala okwanilitsa chilamulo. Izi zikutheka bwanji? Patapita masiku asanu ndi atatu Yesu atabadwa, makolo ake anapita naye ku Yelusalemu komwe anamuchita mdulidwe monga mwachilamulo cha Mose ndipo anamutcha dzina loti Yesu momwe analonjezera ngelo uja. Izi zinachitika kukwaniritsa malemba. Mavesi omwewa akuwonetsera kuti kubadwa kwa Yesu kunali kukwanilitsidwa kwa malonjezo a mulungu. Ngelo wa mulungu ataonekera kwa Maria anamulonjeza kuti azakhala ndi mwana ndipo mwanayo azamutcha dzina lake Yesu. Mavesi awa akuonetsera kuti zinachitikadi malingana ndi lonjezolo ndipo mwanayo anamutchadi Yesu. Chinthu china chofunikira kudziwa chomwe mavesi awa akukamba ndi ichi, Yesu ndi nkhoswe ya anthu onse okhala pa dziko. Ndime za malembazi zikukamba momveka bwino kuti “mwanayo azakhala kugwa ndi kuzuka kwa ambiri mu Israeli.” Izi zikuonetsera kuti Yesu ndi nkhoswe ya anthu padziko. Iye ndi njira yokhululukira machimo athu. Nthawi zonse ndime za malemba ngati izi zimatilimbikitsa ife kutsendera chifupi ndi mulungu podzindikira kuti tili ndi nkhoswe yokhululuka machimo athu. Luke 2:21-35 this passage exposes three important things which are worthy discussing. This passage talks about Jesus being the fulfillment of the law. How so? Eight days after Jesus’ birth, his parents took him to Jerusalem where he was circumcised per the law of Moses. And they named him Jesus according to what the angel said they were to name him. This happened in fulfillment of the scriptures. These verses also show that the birth of Jesus happened in fulfillment of promises made by God. After the angel appeared to Mary he promised her that she would give birth to a son and she is to name him Jesus. And these verses show that it happened exactly as the angel promised and Mary and Joseph named the child Jesus. One more thing to take note of from these verses is that Jesus is the propitiatory sacrifice for all people on earth. The verses say that “the child will be the down fall and the rising of the many in Israel.” This clearly paints the picture of the one who atones the sins of the many on earth. He is the way that many sins are forgiven. Every time we learn something like this from the scriptures we are encouraged. It draws us ever closer to God knowing that we have someone who atones for our sins and we can therefore approach the throne of Grace.

Duration:00:40:30

Ask host to enable sharing for playback control

Mulungu amalamulira mbiri ya anthu/God controls human history

12/29/2023
Luka 2:1-20 tsiku la Christmas ndi tsiku la kubadwa kwa mfumu yodzichepetsa. Ndime yamalembayi ikuonetsa bwino lomwe momwe ulosi wakubadwa kwa mesiya unakwanilitsidwa. Ikutionetsanso kuti obadwayo ndi ochokera ku masiku amake dzana, ndipo ndi mulungu ndithu kubadwira mumbiri ya anthu. Ndime yamalembayi ikuyamba ndi lamulo lochokera kwa Kayisara Augusto. koma ndichifukwa chiyani lamuloli lili lofunika? Tili ndi ulosi kale omwe ukukamba komwe mesiya azabadwire koma n’kuti pa nthawiyi Maria ndi Yosefe akukhala ku Galileya ku Yudeya. Izi zikuonetsa kuti ngati Maria angabereke pa nthawiyi, kuberekako kuchitikira ku Yudeya. Koma mesiya akuyenera kubadwira ku Betelehemu muzinda wa Davide molingana ndi ulosi. Izi ndizofunika kwambiri chifukwa mfumu yodzichepetsayi ikuyenera kuzalowa ufumu wa bambo ake Davide. Kubadwa kudzera mwa Maria ndi Yosefe komanso kubadwira ku Betelehemu zinali zoyenera. Koma kodi zitheka bwanji? Apa ndipamene tingaziwe kuti mulungu mu mphamvu ndi ulamuliro wake amalamulira mbiri ya anthu. Zotsatira zake tikuona Kayesara Augusto akupereka lamulo. Lamulo limeneli lipangisa Yosefe kubwerera kwawo ku Betelehemu pamodzi ndi mkazi wake Maria. Ndipo ali kumeneko ndipamene mesiya akubadwa. Izi zinachitika motere kukwanilitsa malemba ndi ulosi omwe unaneneratu za kubadwa kwa mesiya. Luke 2:1-20 the day of Christmas is the day of the birth of a lowly king. This passage paints a clear picture for us as we see a prophecy about the birth of Messiah being fulfilled. It also helps us to understand that the one to be born is from ancient of days. it is God himself being born into human history. Now, the passage begins with a decree made by Caesar Augusto. How is that decree important? We already have a prophecy that tells us exactly where the messiah would be born but at this time we see Mary and Joseph staying in Galilee in Judea. It obviously means that if Mary were to give birth, it would happen in Judea. But the messiah must be born in Bethlehem, the city of David. This is important because the lowly king is to succeed the throne of his father David and his birth through Mary and Joseph and in Bethlehem are just the right circumstances. But how will it happen? This is where we understand that God in his divine providence controls everything. That’s why the decree made by Caesar Augusto is important. This will cause Joseph to go back to his village in Bethlehem obeying the decree. He goes there with his wife and while there it is when Mary gives birth to the lowly king Jesus Christ. This happened to fulfill what was already prophesied about the birth of the messiah.

Duration:01:14:43

Ask host to enable sharing for playback control

Mphamvu ndi chisankho cha mulungu/Selection and sovereignty of God

12/27/2023
Luka 1:57-80 ikukamba zokhuza chithu chapadera chokhuza mulungu chimene mavesi ena a muchaputa ichi akamba kale. Kufotokozera komwe kwapelekedwa kale kukugwirizana ndi maulosi ena omwe amakamba za kubadwa kwa mesiya. Mulungu amasankha mu mphamvu yake yemwe akufuna kumugwiritsa ntchito pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Tsopano kuti timvetse zokhuza mphamvu ndi chisankho cha mulungu, mavesi a 57-80 a Luka akuyankhulapo momveka bwino pa zimenezi. Choyamba, mulungu akusankha mtsikana ozichepesa osauka ochokera kumnzinda osaziwika yemwe dzina lake ndi Maria. Ngelo Gabriel ochokera kwa mulungu anapereka uthenga kwa Maria kuti azakhala ndi pakati pa mzimu ndipo mwana obadwayo azakhala mwana wa wam’mwamwambayo. Maria anayilandira nkhaniyi ndipo anafuna kuwuza m’bale wake Elizabeti. Koma ngelo uja asanapite anamuuza Maria za m’bale wakeyo kuti anali ndi pakati mu ukalamba wake chifukwa sankabereka. Iye anachita izi kumusimikizira Maria kuti palibe chomukanika mulungu. Chachiwiri, mulungu akukamba momveka bwino malo, nthawi komanso motani momwe mwanayo azabadwire. Maulosi amanena kuti mwanayo azabadwira ku mnzinda wa Betelehemu mudzi wa Davide ndipo ndi komwe anabadwira. Mulungu akuwonetsetsa kuti zichitike malingana ndi ulosi wake ndipo zinachitikadi. Izi zimatithandizira kuzindikira kuti mulungu ndi wamphamvu zonse ndipo amalamulira zonse zochitika pa dziko lapansi. Tsopano, kudziwa izi zokhuza mulungu, zitanthauzanji kwa ife? Izi zimathandizira ife kudziwa kuti mulungu samasintha. Iye anali mulungu yemweyo munthawi yakale, iye ali mulungu yemweyo munthawi yatsopanoyi komanso apitiriza kukhala mulungu yemweyo munthawi yakutsogolo ndipo tikhoza kumudalira chifukwa samakhumudwitsa. Luke 1:57-80 talks about something special about God that other verses of this chapter have already discussed. The explanation given here agrees perfectly with all the other prophecies foretelling the birth of messiah. God chooses whomever he wants to use in order to fulfill his purposes. Now to understand clearly about selection and sovereignty of God, verses 57-80 of Luke makes a clear comment on that issue. Firstly, God chooses a noble village girl called Mary who is lowly and poor from a small town. Angel Gabriel from God appears to Mary and gives her the news that she will conceive a child with the power of the spirit from God and the child to be born will be called the son of the highest God. Mary accepts the great news and wants her cousin Elizabeth to know. But before the angel goes back to heaven, he tells her about Elizabeth who also has conceived a child in her old age because she was known to be barren. The angel does this to assure her that nothing is impossible to God. Secondly, God makes it clear how, where and when the messiah would be born. Prophecies foretell that the child would be born in a small town called Bethlehem, the city of David and that’s exactly where the child is born. This helps us to understand that God is sovereign and that he controls every event that unfolds on earth. Now, knowing that about God, what does it mean to us? This helps us to understand that God never changes. He was the same God in the past, he is the same God in the present and he continues to be the same God in the future and we can trust him completely because he never disappoints.

Duration:00:38:33

Ask host to enable sharing for playback control

Mulungu akonda anthu ake powapatsa mpulumutsi/God gives his people a savior out of love

12/25/2023
Luka 1:39-45 Maria azonda Elizabeti. Nthawi imene Maria anapereka moni kwa Elizabeti, yemwe anali oyembekezera pa nthawiyo, mwana m’mimba mwake anadumpha ndi Chimwemwe. Elizabeti anali ndi kuthekera kodziwa chinthu chapadera chokhuza mwana yemwe Maria anali m’mimba mwake. Tikuyenera kudziwa izi zokhuza Elizabeti, iye anadziwa bwanji kuti Maria anali atayembekezera ambuye? Malemba amawonetsa kuti iye anali wodzadzidwa ndi mzimu wa mulungu. Izi zinapangisa kuti iye adzindikire bwino za mwana ameneyu. Chinthu chofunikira kudziwa ndi ichi, mulungu amachita zinthu zikuluzikulu myoyo yathu ngati ife timudalira iye ndi chikhulupiriro. Elizabeti anadalira mulungu moyo wake ndipo mulungu anamuzindikiritsa iye kuti Maria anali oyembekezera mpulumutsi wa anthu onse pa dziko. Maria yemwe anali ozichepesa pamaso pa mulungu anasankhidwa kubereka ambuye, zomwe ndi zinthu zopasa chidwi. Mulungu amagwiritsa ntchito anthu omwe ndi opanda kanthu kalikonse ku dziko kuti akwaniritse zolinga zake ndi kulemekeza zina lake. Mulungu amagwiritsa ntchito anthu omwe ndi opanda kanthu komanso ndi osaukitsitsa kuti achite zolinga zake ndi kulemekeza zina lake. Chimodzimodzi ife Akhristu lero, amene ndi osauka mu uzimu komanso opanda kanthu, mulungu angatigwiritse ntchito ngati timulora iye kuti atero. Choncho tiyeneni tizipereke kwa mulungu kwa tunthu kuti atigwiritse ntchito mu utumiki wake. Luke 1:39-45 Mary visits Elizabeth. When Mary greets Elizabeth, who was pregnant at this time, the child in her womb made sudden movements showing happiness. Elizabeth is able to notice something special about the child Mary was carrying in her womb. There is something to be noted about Elizabeth, how was she able to know that Mary was carrying the lord in her womb? The scriptures show that she was filled with the holy spirit from God. This enabled her to know who this child was even before he was born. This makes Elizabeth’s child happy upon hearing the greeting from Mary. One thing important to take note of is that God can make great things in life happen to us but only if we believe in him and trusts him completely. Elizabeth trusted the lord and was given the privilege to know that Mary was carrying a child who literally would be the lord and savior of mankind. Mary from humble beginning was called by God to give birth to the lord, something which is remarkable. God uses those who are nothing in the eyes of the world to bring about his purposes and glorify his name. God uses people who are poor and lowly to accomplish his will and glorify his name. The same applies to us Christians who are lowly and poor in spirit, God can use us to accomplish his purposes and glorify his name. So we should be open and allow him to use us in his ministry.

Duration:00:35:24

Ask host to enable sharing for playback control

Nkwabwino kukhala olimba muchikhulupiriro/It is good to remain firm in the Faith

12/4/2023
Luka 1:26-38 ikutibweretsera nkhani ya msungwana wosaziwa mwamuna otchedwa Maria ndipo amakhala mu zinda wa Nazareti ku Galileya. Msungwana ameneyu analibe kudziwika kulikonse, analibe chilichonse chopatsa chidwi komanso amakhala muzinda wosatchuka. Koma mulungu anali naye cholinga msungwanayu. Ngelo Gabrieli anabweretsa nkhani yabwino nati “uzakhala ndi pakati ndipo uzabereka mwana wamwamuna. Ndipo uzamutche Yesu.” Kubadwa kwa Yesu, kapena kunena kuti kubadwa kodzichepetsa kwa Yesu kunabwera kudzera mwa Maria. Koma mkati mwakukambirana ndi ngeloyo Maria anachita mantha. Izi zimachitika iye atalandira chitomero kuchokera kwa mwamuna otchedwa Yosefe wa fuko la Davide. Kukambirana kwawo kutatha Maria anamvetsetsa kuti ichi chinali chisankho cha mulungu ndipo iye sakanatha kutsutsa. Izi zinali motere chifukwa ankadziwa zina zokhuza mulungu. Zomwe ndizopatsa chidwi mukukambirana kwawo ndi momwe Maria anamuyankhira ngeloyo. Iye anati “zichitike monga momwe mwanenera. Popeza ine ndi mtumiki wa ambuye.” M’mawu ake, iye akuwonetsa kukula kwa chikhulupiriro chake pa mulungu. Iye akutiphunzitsa kulemekeza zisankho zomwe mulungu amatipangira ife ngati ana ake komanso osankhidwa ake. Monga ana a mulungu, ngakhale tikumane ndi mavuto oopsa, titsatire chitsanzo chabwino cha chikhulupriro cha Maria. Tikhale ndi mtima okwanitsa kunena kuti ‘zikhale monga momwe ambuye mufunira.’ Luke 1:26-38 brings us a story of a young virgin named Mary who lived in a small town of Nazareth in Galilee. This young woman had no publicity, had nothing interesting and was living in a place not famous. But God had a plan for her. Angel Gabriel brought her news saying “you will be pregnant and give birth to a son. And you will name him Jesus.” The birth of Jesus, also known as a humble birth of Jesus came about through this young woman called Mary. In the midst of all this, Mary was terrified and was afraid. At this point already, she had received a marriage proposal from a man called Joseph of the clan of David. After conversing with angel Gabriel, Mary finally understood and agreed to it, for this was God’s choosing and she had no objection. This was so, because she understood things concerning God. What’s interesting is how she responded to the angel. She said to the angel ‘let it be as you have said, for I am the servant of the lord.’ In her words, she expressed a tremendous amount of faith in God. She teaches us how to value the choices that our creator makes for us as his chosen ones and his children. As the children of God, in every circumstance that we face whether good or bad in his ministry, we should imitate Mary’s faith. We should learn to say that ‘let it be as the lord has purposed it.’

Duration:00:52:01

Ask host to enable sharing for playback control

khalani anthu okonda chilungamo/Be a people that love justice

11/27/2023
Mateyu 5:21-26 ikupitiriza kuyankhula zokhuza chilungamo. Ndipo chilungamo chimene mulungu akufuna, sichakunja ayi koma chankati mwa munthu. Yesu akuyankhula kunena kuti ‘ngati chilungamo chanu sichiposa cha afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, simuzalowa mu ufumu wakumwamba.’ Mu zoyankhula zina,Yesu akuyamba mayankhulidwe ake kunena kuti “munamva kunanenedwa kuti.” Kuchoka pamenepo iye akuyankhula ndi kuwaonetsa anthu zokhuza chilamulo cha Mose. Komanso akuwawonesera momwe angatsatirire chilamulo chimenechi. Kenako akubwerera ku nthawi yatsopano kuti afotokoze momwe amayenerera kumvetsetsera chilamulo chimenechi. Kodi ndi zofunika bwanji kuti iye akambe zimenezi? Yesu watiwuza kale kuti sanabwere kuzathetsa chilamulo ndi aneneri koma kuzakwaniritsa. Yesu akutiwuza kunena kuti chilungamo chanthu chisangokhala cha kunja kokha koma chizichokera mkati mwathu. Potengera ndi zomwe chilamulo chimafuna kuti tizichita, ndi Yesu yekha amene anakwaniritsa kukhala moyo omvera chilamulo chimene mwangwiro. N’chifukwa chake akutiwuza momwe tingatsitirire chilamulo chifukwa iye ndiye amene akudziwa bwino lomwe. Yesu akutipempha kuti tikhale anthu okonda chilungamo. Ndipo chilungamo chathu chiwale ngati muni kuti onse omwe awona kuwalako alemekeze atate athu akumwamba. Chilungamo chathu chisakhale chakunja kokha kuti ena atitamandire ife. Matthew 5:21-26 continues to talk about justice. And the type of justice that God wants, is not the outward justice but the inward justice. Jesus makes a statement about this saying that ‘if your righteousness does not surpass that of the Pharisees and the teachers of the law, you will by no means enter the kingdom of the heavens.’ Now, in his statements, Jesus begins most the sentences with the word “you heard that it was said.” And from there, he goes back to the old testament and show people what the law of Moses is about and also show them how they should live by it. And then he goes back to present time and show the people how they should understand the law of Moses. How important is it that he explains the law? Earlier, Jesus has already told us that he didn’t come to abolish the law and the prophets but he came to fulfil it. So, Jesus shows us that justice shouldn’t be a thing of outside but should involve inside life. And looking at what the law requires us to do, the only one who can follow the law perfectly is Jesus. Jesus in his entire life lived in obedience to the law. And that is why he tells us how to follow the law because he knows how. Jesus invites us to exercise true righteousness. Let it shine like light before men, and those who see it will glorify our heavenly father. Our righteousness shouldn’t be a thing of outside appearance in order to be praised by others.

Duration:00:49:41

Ask host to enable sharing for playback control

Yesu aphunzitsa ndi ulamulilo/Jesus teaches with authority

11/20/2023
Mateyu 7:24-29 Yesu akuyamba vesi 24, kunena kuti ‘yense omva mawu anga.’ Izi ndizofunika kuzisunga, chifukwa zithandizira ife kumvetsa bwino chifukwa chimene anthu omvera ulaliki wake ananena kuti amayankhula ngati yemwe anali ndi ulamuliro. Osati ngati aphunzitsi amalamuliro. Anthu ambiri analondola Yesu. Ndipo iye anakwera paphiri nayamba kuphunzitsa ophunzira ake. Mu mavesi a 24-29, yesu akuyankhula za munthu wanzeru ndi opusa. Awafotokoza motere; munthu wanzeru ndi amene amamva mawu ake ndi kuwachita. Kenako akulumikizisa ndi munthu yemwe akumanga nyumba yake pa tanthwe. Mvula inabwera koma nyumba sinagwe chifukwa inamangidwa polimba. Njira iyi ndi yomwenso Akhristu akuyenera kugwiritsa ntchito kumanga chikhristu chawo. Akhristu akuyenera kumanga pa tanthwe limene ndi Yesu Khristu. Ndipo iye akulonjeza kuti ndi maziko omwe sadzagwetsedwa konse. Ndipo pamapeto iye akumaliza ndi munthu opusa. Munthu opusa akumanga nyumba yake pa mchenga. Mvula inabwera ndipo nyumbayi inagwa. Zitsanzo zonsezi zimamveka bwino kunena kuti, wanzeru ndi munthu amene amamva mawu a Yesu ndi kuwachita ndipo munthu uyu ndi odala, Mateyu 5. Izi ndi zosiyana ndi munthu yemwe amamva mawu a Yesu ndipo samawachita. Zimangowonetsa kuti munthuyu sanamve konse mawu a Yesu. Ndiponso munthuyu sanali Khristu kumayambiriro komwe. Ndipo izi zimamupanga iye kukhala munthu opusa. Mayankhulidwe oterewa ndi omwe angayankhulidwe ndi yemwe ali ndi ulamuliro. Ndi chifukwa anthu anati, akuyankhula ngati munthu yemwe ali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo. Mathew 7:24-29 Jesus begins verse 24, saying ‘whoever hears my word.’ Now, we have to take note of this because that will help us to understand why the crowd listening to him concluded saying that ‘he spoke as someone with authority. Not like the teachers of the law.’ A huge crowd followed Jesus. And Jesus gets on a mountain and sits down and opened his mouth to teach his disciples. In verses 24-29, Jesus talks about someone who is wise and someone who is foolish. He describes them this way; a wise person is the one who hears his word and does it. And from there he links it with someone who builds a house on a rock. Jesus said that, the rains came, the wind blew and the flood water lashed against this house but it was founded firm and it remained. And this applies to how true Christians are to build their houses which is their Christianity. Christians are to build on the true foundation which is Jesus Christ. And Jesus assures his people that no matter what problem they may face, they never will be destroyed for they are founded on the true foundation which is Jesus. And finally, Jesus concludes talking about a foolish person. Now, this person is foolish because he builds his house on sand and the rains come and lashes against this house and it is destroyed. Now all these two examples are understood clearly this way; Jesus talks about his word, the one who hears his word and does it is blessed, Matthew 5. in simple terms, this person hears and does it and is a happy person. This is unlike with someone who hears and does not do Jesus word. In simple terms, it just shows that this person never heard the word of Jesus. And never was a Christian to begin with, this makes that person a fool. It is only someone with authority who can speak like that, thus why the people concluded that he spoke like someone with authority not like the teachers of the law.

Duration:00:38:25

Ask host to enable sharing for playback control

Mzimu woyera anatsekulira njira anthu amitundu kuti akhulupirire uthenga wabwino/The holy spirit opened the door for gentiles to believe the Gospel

11/16/2023
Mateyu 5:17-20 Yesu akwera pa Phiri ndipo akhala pansi ndikuyamba kuphunzitsa ophunzira ake ngati Mose watsopano ndi opereka lamulo watsopano. Funso nali, funso limene limazunguza anthu ambiri; kodi ndi ubale wanji omwe ulipo pakati pa lamulo la Khristu ndi la muchipangano chakale? Pofuna kuyankha funso limeneli, chiyambi cha vesi ya 17 ya chaputachi imapereka yankho lomveka bwino. Yesu anti “musaganize kuti ndinabwera kuzathetsa chilamulo ndi aneneri. Sindinabwere kuzathetsa koma kudzakwaniritsa.” Tsopano, chaputa cha 1, 2, 3, 4 cha Mateyu muli zolemba zomwe zimasonyeza kukwaniritsidwa kwa kubwera kwa Mesiya. Mwa chitsanzo, mwana Yesu anatengeredwa ku Igupto pofuna kukwaniritsa zomwe zinalembedwa zonena kuti ‘ndinamuitana mwana wanga kuchoka ku Igupto.’ Izi zikuonetsa kuti Yesu sanabwere kuzathetsa chilamulo ndi aneneri koma kuzakwaniritsa zonse zomwe zinalembedwera iye, zokhuza iye. Koma, kodi chilamulo, aneneri ndi zolembalemba zinangoperekedwa kwa Ayuda popanda chifukwa? Kapena inangokhala njira yonena kuti iwo azizitukumulira? Ayi! Chilamulo komanso aneneri zinaperekedwa kwa iwo ngati njira yowakonzekeretsa za kubwera kwa Mesiya. Ndiye, tinene kuti chilamulo ndi aneneri zikuphunzitsa ife kuti tizinyoza ena omwe samatsatira kadyedwe ka Ayuda? Kapena chifukwa samapembeza tsiku lofanana ndi lomwe inu mumapembezera? Kapena chifukwa samasunga sabata momwe inu mumachitira? Yesu akutitsimikizira kuti anabwera kuzapulumutsa Ayuda ndi Amitundu. Izi zikuoneka bwanji? Mzimu woyera amatsekulira njira amitundu kuti amve ndi kukhulupirira uthenga wabwino wa Yesu Khristu ndikulandira chipulumutso. Matthew 5:17-20 Jesus gets on a mountain and sits down to teach his disciples as the new Moses and the new law giver. Now the question that has many people wonder so much is; what is the relationship of the law of Christ to the law of the old testament? To answer that question, the beginning of verse 17 of this chapter clears our minds with what Jesus himself said. Jesus said “don’t think that I came to abolish the law or the prophets. I did not come to abolish but to fulfill.” Now, chapters 1, 2, 3, 4 of Matthew records all the accounts that took place in fulfilment of the coming of Messiah. For example, baby Jesus was taken to Egypt to fulfill what was written saying that ‘I called my son out of Egypt.’ This shows us that Jesus indeed came to fulfill what was written about him and for him and not to abolish the law and the prophets. But, was the law, the prophets and the writings given to the Jews for no good reason at all? Or was it just for them to brag that they had the law and the prophets? No! the law and the prophets were given them as a way of preparing them for the coming of messiah. So, does the law and the prophets teach us to view others lesser because they’re unable to follow the diet of the Jews? Or because they do not worship on a certain day like you do? Or that they do not keep the Sabbath according to your point of view? Jesus tells us clear that he came to save all, whether Jew or Gentile. Where do we see this? The holy spirit opens the door for Gentiles to hear and believe the Gospel of Jesus Christ and receive salvation.

Duration:00:49:42

Ask host to enable sharing for playback control

Tinalengedwa kuti tizipembedza mulungu/We were created to worship God

9/18/2023
Genesis 19:1-14 in this passage we see that the only sin that is making the head lines is homosexuality. Now if we look deeper we would see that many sins are committed. Sins like not being hospitable to the guest who came to Lot’s house, being violent in trying to get a hold of the angelic men but even more the people of Sodom have denied their nature to worship God. So, God gives them away to all this kind of sins that they are committing. Now this helps us to understand where we are basing our foundation as Christians. We got to be more careful because it is our nature to worship God. If we happen to deny worshiping God, then that means we are choosing to worship something else. And it is obviously termed as idol worshiping which brings about the wrath of God. And as if that is not enough we start to become like the idols that we are worshiping which results into this sin of homosexuality. So, because we have become like animals, we no longer care about what’s right and what’s wrong for that is no longer in our nature. Because we have denied worshiping God. Genesis 19:1-14 mu ndime ya malembayi tikuona kuti tchimo lomwe lamanga nthenje ndi la kugonana amuna okhaokha komanso akazi okhaokha. Koma tikaonetsetsa mkati bwino lomwe tikupeza kuti machimo ambiri akuchitidwa. Monga ngati kuonetsa kusalandira alendo omwe anabwera ku nyumba ya loti, kuchitira nkhanza alendowa. Koma kuonjezera pamenepo tchimo lalikulu kwambiri limene anthu amumzinda wa Sodomu achita ndi kukana kupembeza mulungu. Ndipo mapeto ake mulungu akuwapereka ku machimo awo. Izi zikuthandizira ife ngati akhristu kudziwa pomwe tikumangira madziko a moyo wathu. Tikuyenera kukhala osamala chifukwa ndi chikhalidwe chathu kupembedza mulungu. Ngati tisankha kukana kupembedza mulungu, ndiyekuti tikusankha kupembedza winawake. Ndipo kutero ndikupembedza mafano, kumene kumabweretsa mkwiyo wa mulungu. Kuonjezera pamenepo timayamba kusandulika kukhala mafano omwe tikupembedzawo ndipo mathero ake ndikuchita zinthu ngati nyama. Nyama zomwe sizisamala chabwino ndi choyipa chifukwa sichikhalidwe chake kutero. Chifukwa takana kupembedza mulungu.

Duration:00:46:34

Ask host to enable sharing for playback control

Mtengo wapatali wakukhala ophunzira/The cost of discipleship

9/15/2023
Mateyu 5:5 kuyankhula mwachidule, chipulumutso ndichaulere. Mwazi wa Yesu Khristu unagula chipulumutso. Timangoyenera kulapa ndi kutembenuka mtima kusiya machimo ndi kukhulupirira uthenga wabwino kuti tilandire chipulumutso. Komabe sizikutanthauza kuti munthu opulumutsidwa samalipira konse, ayi! M’malo mwake amalipira pamene alapa machimo ndi kutembenuka mtima ndi kumutsata Yesu Khristu. Yesu akutichenjeza mu uthenga wabwino kuti tilingalire mozama za kukhala ophunzira wa Yesu. Iye akunena kuti ‘yense ofuna kusunga moyo wake azawutaya koma yense yemwe ataya moyo wake azawupeza chifukwa cha zolinga za Yesu Khristu.’ Matthew 5:5 to say in brief, salvation is for free. It was purchased by the blood of Jesus Christ. All we need to do is to repent of our sins and believe the gospel of Jesus and we will have salvation. But of course, it doesn’t mean that there is no cost, the cost is that a believer pays the cost as he turns away from his sins and follow Jesus. For Jesus teaches us in the gospel that we should consider the cost of discipleship. He says that ‘everyone who saves his life will lose it but whoever loses his life will save it for the sake of Jesus Christ.’

Duration:00:42:56

Ask host to enable sharing for playback control

Mulungu ndi wabwino ndi wolungama/God is good and righteous

9/11/2023
Genesis 18:16-33 mulungu akuonetsera chilungamo chake pamene anthu akuchita zosutsana naye. Mulungu walinganiza zowononga Sodomu chifukwa cha uchimo wawo koma muzonsezi mulungu akukhalabe olungama. Chifukwa mulungu akuonetsera chilungamo chake mwa Abrahamu, zimene iyeyo ali ngati mulungu kuti iye amadalitsa komanso iye amawononga, iye amatembelera, iye amalanga. Mulungu waonetsera madalitso ake pa Abrahamu pochita naye malonjezo ndi kuwakwaniritsa. Tsopano mulungu akufuna kumuonetsera Abrahamu kuti iye ngati mulungu amalanga onse ochita zoyipa. Kodi ife tikusankha kukondweletsa mulungu kapena zokhumba zathu ndi zomwe zili pa sogolo? Ngati ndi choncho kodi tikudziwa kuti mulungu ndi olungama ndipo sazalora kuti tchimo lipite osalangidwa! Kodi nanga ife tili pati? Genesis 18:16-33 God shows his great righteousness when people are up against him. God has spoken out the distraction of Sodom because of their great sins and in all of this God remains righteous. God demonstrates his righteousness through Abraham that he blesses, judges and he also curses and he punishes. God has shown his blessings through Abraham by making promises with him and fulfilling them. And now God wants to show Abraham that he punishes those who do sin. Are we choosing to please God or are we putting ourselves in the front? If that’s so, did we know that God is righteous and that he will never let sin go unpunished? Now, where are we found?

Duration:00:51:08

Ask host to enable sharing for playback control

Khalani ophunzira weniweni wa Yesu Khristu/Be a true disciple of Jesus Christ

9/8/2023
Mateyu 5:1-3 ndime zamalemba izi ndi zofunika kwambiri kuwunikirana chifukwa ndi gawo limodzi la chiphunzitso chotchuka cha Yesu. Phunziro limene likupezeka mu ndime za malembazi ndi lakuti uthakukhala Nkhristu koma osakhala Nkhristu weniweni. Nkhani siyongopezeka ku malo opembedzera mulungu tsiku la mulungu kapena loweruka koma makamaka kukhala otsatira kapena ophunzira weniweni wa Yesu ngakhale masiku ena onse. Tiyenera kukhala anthu amene tapereka moyo wanthu wonse kwa Yesu , osati maola awiri okha tsiku la sabata lokha ayi koma mphindi iliyonse ya moyo. Matthew 5:1-3 These passages are important to discuss them because they are part of the famous teachings of Jesus Christ called the sermon on the mountain. And part of the lessons of this teaching tells us that you can be a Christian but really not being a Christian. It isn't just about being present at church every Sunday or Saturday and committing your two hour time but it's really about being a true follower of Jesus. It means every minute of your life is committed to being a disciple of Jesus Christ.

Duration:00:41:52

Ask host to enable sharing for playback control

Mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu/God is all knowing and all powerful

9/4/2023
Genesis 18:1-15 Kodi pali chimene ndi chokanika kwa mulungu? Akhristu nthawi zina timayetsedwa kuganiza kuti tili ndi kuthekera komuuza mulungu zomwe iye samadziwa. Koma kodi izi ndi zotheka? M'buku la Genesis 18 likutionetsera kuti mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu. Zonse zimene Abrahamu ndi Sara akudutsa ndi njira imene mulungu wayika kuti awiriwa amudziwe mulungu. Mulungu akudziwa pamene Sara anaseka mulungu atanena kuti azakhala ndi mwana ngakhale Sara sanali pafupi ndi ambuye omwe anabwera kwa Abrahamu ndi angelo awiri. Ndi mavuto anji, ndi mtenda yanji kapena ndi chiyani chikusowetsa mtendere moyo wanu? Dziwani kuti zonsezi timadutsa ndi cholinga choti mulungu adzivumbulutse yekha kwa ife momwe anachitira ndi Abrahamu. Kodi inu mudalira mulungu? Genesis 18:1-15 Is anything impossible for God? Christians sometimes are tempted to think that they can tell God what they think he doesn't know about them. Is that even possible? Genesis 18 tells us that God is all knowing and all powerful. All that Abraham and Sarah are going through is for them to know God. God is aware when Sarah laughs after he had said that she will have a baby even though Sarah wasn't there with them. All the circumstances that these two are facing are there to help them know God and trust him. What problems are you facing, what diseases are battling, know that through it all God wants us to know him. So! Will you trust him?

Duration:00:44:21